7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva cisoni cifukwa ndapanga izo.
8 Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.
9 Mibadwoya Nowandiiyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yace; Nowa anayendabe ndi Mulungu.
10 Ndipo Nowa anabala ana amuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.
11 Ndipo dziko lapansi linabvunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi ciwawa.
12 Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linabvunda; pakuti anthu onse anabvunditsa njira yao pa dziko lapansi.
13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Cimariziro cace ca anthu onse cafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi ciwawa cifukwa ca iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.