7 Ndipo analowa Nowa ndi ana ace ndi mkazi wace ndi akazi a ana ace m'cingalawamo, cifukwa ca madzi a cigumula.
8 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,
9 zinalowa ziwiri ziwiri kwa Nowa m'cingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
10 Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a cigumula anali pa dziko lapansi.
11 Caka ca mazana asanu ndi limodzi ca moyo wa Nowa, mwezi waciwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi akuru anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
12 Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.
13 Tsiku lomwelo analowa m'cingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wace wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ace pamodzi nao: