17 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ici ndici cizindikiro ca pangano ndalikhazikitsa popaogana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.
18 Ndi ana amuna a Nowa amene anaturuka m'cingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wace wa Kanani.
19 Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.
20 Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa:
21 namwa vinyo wace, naledzera; ndipo anali wamarisece m'kati mwa bema wace.
22 Ndipo Hamu atate wace wa Kanani, anauona umarisece wa atate wace, nauza abale ace awiri amene anali kunja.
23 Semu ndi Yafeti ndipo anatenga copfunda, naciika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda cambuyo, napfunditsa umarisece wa atate wao: nkhope zao zinali cambuyo, osaona umarisece wa atate ao.