26 Koma amuna awiri anatsalira m'cigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzace ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanaturuka kumka kucihema; ndipo ananenera m'cigono.
27 Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'cigono.
28 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wace, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.
29 Koma Mose anati kwa iye, Kodi ucita nsanje nao cifukwa ca ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! mwenzi Yehova atawaikira mzimu wace!
30 Ndipo Mose ndi akulu onse a Israyeli anasonkhana kucigono.
31 Ndipo kudacokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zocokera kunyanja, nizitula kucigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa cigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.
32 Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wace wonse, ndi mawa lace lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa cigono.