23 Ndipo anadza ku cigwa ca Esikolo, nacekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.
24 Malowa anawacha cigwa ca Esikolo, cifukwa ca tsangolo ana a lsrayeli analicekako.
25 Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai.
26 Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ku cipululu ca Parana ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
27 Ndipo anafotokozera, nati, Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu a moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndi zipatso zace siizi.
28 Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikuru ndithu: ndipo tinaonakonso ana a Anaki.
29 Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordano.