18 Ndipo nyama yace ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.
19 Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamcere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.
20 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe colowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi colowa cako pakati pa ana a Israyeli.
21 Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israyeli, likhale colowa cao, mphotho ya pa nchito yao alikuicita, nchito ya cihema cokomanako.
22 Ndipo kuyambira tsopano ana a Israyeli asayandikize cihema cokomanako, angamasenze ucimo kuti angafe.
23 Koma Alevi azicita nchito ya cihema cokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale naco colowa pakati pa ana a Israyeli.
24 Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israyeli, limene apereka nsembe, yokweza kwa Yehova, likhale colowa cao; cifukwa cace ndanena nao, Asadzakhale naco colowa mwa ana a Israyeli.