20 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe colowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi colowa cako pakati pa ana a Israyeli.
21 Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israyeli, likhale colowa cao, mphotho ya pa nchito yao alikuicita, nchito ya cihema cokomanako.
22 Ndipo kuyambira tsopano ana a Israyeli asayandikize cihema cokomanako, angamasenze ucimo kuti angafe.
23 Koma Alevi azicita nchito ya cihema cokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale naco colowa pakati pa ana a Israyeli.
24 Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israyeli, limene apereka nsembe, yokweza kwa Yehova, likhale colowa cao; cifukwa cace ndanena nao, Asadzakhale naco colowa mwa ana a Israyeli.
25 Ndipo Yehova ananena ndil Mose, nati,
26 Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israyeli, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale colowa canu cocokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.