6 Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa mota irikupsererapo ng'ombe yamsoti.
7 Pamenepo wansembe atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi; ndipo atatero alowenso kucigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
8 Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
9 Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe ya msotiyo, nawaike kunja kwa cigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a lsrayeli akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yaucimo.
10 Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe ya msoti atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israyeli, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.
11 Iye wakukhudza mtembo wa munthu ali yense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;
12 iyeyo adziyeretse nao tsiku lacitatu, ndi pa tsiku lacisanu ndi ciwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lacitatu, sadzakhala woyera tsiku lacisanu ndi ciwiri.