31 ndi Asiriyeli, ndiye kholo la banja la Aasiriyeli; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;
32 ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Heferi, ndiye kholo la banja la Aheferi.
33 Ndipo Tselofekadi mwana wa Heferi analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
34 Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.
35 Ana amuna a Efraimu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekeri, ndiye kholo la banja la Abekeri; Tahana, ndiye kholo la banja la Atahana.
36 Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani.
37 Iwo ndiwo mabanja a ana a Efraimu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.