52 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
53 Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale colowa cao.
54 Ocurukawo, uwacurukitsire colowa cao; ocepawo uwacepetsere colowa cao; ampatse yense colowa cace monga mwa owerengedwa ace.
55 Koma aligawe ndi kucita maere; colowa cao cikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao,
56 Agawire ocuruka ndi ocepa colowa cao monga mwa kucita maere.
57 Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Gerisoni, ndiye kholo la banja la Agerisoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.
58 Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akohati. Ndipo Kohati anabala Amiramu.