1 Pamenepo anayandikiza ana akazi a Tselofekadi mwana wa Heferi, ndiye mwana wa Gileadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.
2 Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga, ndi khamu lonse, pakhomo pa cihema cokomanako, ndi kuti,
3 Atate wathu adamwalira m'cipululu, ndipo sanakhala iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zace zace; ndipo analibe ana amuna.
4 Licotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lace, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathu lathu pakati pa abale a atate wathu.