21 pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'cuuno mwako, ndi kukutupitsa mbulu;
22 ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa mbulu ndi kuondetsa m'cuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.
23 Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.
24 Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.
25 Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.
26 Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.
27 Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nacita mosakhulupitika pa mwamuna wace, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa mbulu, ndi m'cuuno mwace mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wace.