1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonieza cowinda ca Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;
3 azisala vinyo ndi kacasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kacasu wosasa, kapena cakumwa conse ca mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
4 Masiku onse a kusala kwace asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zace kufikira khungu lace,
5 Masiku onse a cowinda cace cakusala, lumo lisapite pamutu pace; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lace zimeretu.
6 Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.
7 Asadzidetse ndi atate wace, kapena mai wace, mbale wace, kapena mlongo wace, akafa iwowa; popeza cowindira Mulungu wace ciri pamutu pace.