14 Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitirize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuruyo, limene liwazinga.
15 Ndalozetsa nsonga ya lupanga ku zipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kucuruke; ha! analituula linyezimire, analisongoza liphe,
16 Udzisonkhanitsire pamodzi, muka ku dzanja lamanja; undandalitsa nkhondo kumuka kulamanzere; kuli konse ilozako nkhope yako.
17 Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena.
18 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
19 Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babulo; zonse ziwiri zicokere dziko lomwelo; nulembe cizindikilo colozera, ucilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi.
20 Uiike njira yodzera lupanga kumka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.