15 Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m'maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikucokere.
16 Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
17 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
18 Wobadwa ndi munthu iwe, nyumba ya Israyeli yandikhalira mphala; onsewo ndiwo mkuwa, ndi seta, ndi citsulo, ndi ntobvu, m'kati mwa ng'anjo; ndiwo mphala zasiliva.
19 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwasanduka mphala nonsenu, cifukwa cace taonani, ndidzakusonkhanitsani m'kati mwa Yerusalemu.
20 Monga asonkhanitsamtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi ntobvu, ndi seta, m'kati mwa ng'anjo, kuzibvukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani.
21 Inde ndidzakusonkhanitsani, ndi kukubvukutirani ndi moto wa kuzaza kwanga, ndipo mudzasungunuka pakati pace.