1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, ndiye mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
3 nunenere motsutsana naye, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
4 ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'cibwano mwako ndi zokowera, ndi kukuturutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo obvala mokwanira onsewo, msonkhano waukuru ndi zikopa zocinjiriza, onsewo ogwira, bwino malupanga;
5 Perisiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi cikopa ndi cisoti cacitsulo;
6 Gomeri ndi magulu ace onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ace onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe.
7 Ukonzekeretu, Inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao.