1 Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu, ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana amuna, citapita cigumula cija.
2 Ana amuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Mesheki, ndi Tirasi,
3 Ndi ana amuna a Gomeri: Asekenazo, ndi Rifata, ndi Togarma.
4 Ndi ana amuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu.
5 Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa cinenedwe cao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
6 Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, ndi Puti, ndi Kanani.