15 Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ace, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.
16 Ndipo anabwera naco cuma conse, nabwera naye Loti yemwe ndi cuma cace, ndi akazi ndi anthu omwe.
17 Ndipo anaturuka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, ku cigwa ca Save (ndiko ku cigwa ca mfumu),
18 Ndipo Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anaturuka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkurukuru.
19 Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkurukuru, mwini kumwamba ndi dziko lapansi;
20 ayamikike Mulungu Wamkurukuru amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
21 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge cuma iwe wekha.