1 Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
2 Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi Ine ndi iwe, ndipo ndidzacurukitsa iwe kwambiri.
3 Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Yehova ananena naye kuti,
4 Koma Ine, taona, pangano langa liri ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu.