9 Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakucitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe citseko.
10 Komo anthu aja anaturutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo,
11 Ndipo anacititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akuru, ndipo anabvutika kufufuza pakhomo.
12 Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi, ndi onse ali nao m'mudzi muno, uturuke nao m'malo muno:
13 popeza ife tidzaononga malo ano, cifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge.
14 Ndipo anaturuka Loti nanena nao akamwini ace amene anakwata ana ace akazi, nati, Taukani, turukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ace anamyesa wongoseka.
15 Pamene kunaca, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.