2 Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wace mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.
3 Ndipo Abrahamu anamucha dzina lace la mwana wace wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isake.
4 Ndipo Abrahamu anamdula mwana wace wamwamuna Isake pamene anali wa masiku ace asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye.
5 Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isake mwana wace.
6 Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine.
7 Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wace.
8 Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akuru tsiku lomwe analetsedwa Isake kuyamwa.