17 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako.
18 Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwace namwetsa iye.
19 Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.
20 Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wace m'comwera, nathamangiranso kucitsime kukatunga, nazitungira ngamila zace zonse.
21 Munthuyo ndipo anamyang'anira iye, nakhala cete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai.
22 Ndipo panali zitatha kumwa ngamila, munthuyo anatenga mphete yagolidi ya kulemera kwace sekele latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ace, kulemera kwace masekele khumi a golidi.
23 Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi ku nyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife?