2 Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wace wamkuru wa pa nyumba yace, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga:
3 ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana akazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
4 Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isake mkazi.
5 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu kudziko komwe mwacokera inu?
6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Cenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.
7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosacimwa pa cilumbiro cangaci: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.