29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wace dzina lace Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.
30 Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wace, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wace, akuti, Cotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamila pakasupe.
31 Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? cifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamila.
32 Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamila, napatsa ngamila maudzu ndi cakudya, ndi madzi akusamba mapazi ace ndi mapazi a iwo amene anali naye.
33 Ndipo anaika cakudya pamaso pace: koma anati, Sindidzadya ndisananene cimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
34 Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu.
35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo anakula kwakukuru; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golidi, ndi akapolo ndi adzakazi, oeli ngamila ndi aburu.