41 ukatero udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abate anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako.
42 Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;
43 taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene aturuka kudzatunga madzi, ndikati kwa iye, Ndipatse madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;
44 ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamila zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.
45 Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anaturuka ndi mtsuko wace pa phewa lace, natsikira kukasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
46 Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lace, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamila.
47 Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pamphuno pace ndi zingwinjiri pa manja ace.