45 Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anaturuka ndi mtsuko wace pa phewa lace, natsikira kukasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
46 Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lace, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamila.
47 Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pamphuno pace ndi zingwinjiri pa manja ace.
48 Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wace mwana wamkazi wa mphwace wa mbuyanga.
49 Tsopano, ngati mudzamcitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere.
50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Caturuka kwa Yehova cinthu ici; sitingathe kunena ndi iwe coipa kapena cabwino.
51 Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.