14 ndi Misima, ndi Duma; ndi Masa;
15 ndi Hadada, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema;
16 ana a Ismayeli ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akaronga khumi ndi awiri m'mitundu yao.
17 Zaka za moyo wa Ismayeli ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wace.
18 Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwace kwa Aigupto, pakunka ku Asuri: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ace onse.
19 Mibadwo ya Isake mwana wace wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isake:
20 ndipo Isake anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Msuriya wa ku Padanaramu, mlongo wace wa Labani Msuriya.