20 ndipo Isake anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Msuriya wa ku Padanaramu, mlongo wace wa Labani Msuriya.
21 Ndipo Isake anampembedzera mkazi wace kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwace, ndipo Rebeka mkazi wace anatenga pakati,
22 Ndipo ana analimbana m'kati mwace: ndipo iye anati, Ngati cotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.
23 Yehova ndipo anati kwa iye,Mitundu iwiri iri m'mimba mwako,Magulu awiri a anthu adzaturuka m'mimba mwako;Gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzace;Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.
24 Atatha masiku ace akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.
25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwace monga maraya aubweya; ndipo anamucha dzina lace Esau.
26 Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.