21 Ndipo Isake anampembedzera mkazi wace kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwace, ndipo Rebeka mkazi wace anatenga pakati,
22 Ndipo ana analimbana m'kati mwace: ndipo iye anati, Ngati cotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.
23 Yehova ndipo anati kwa iye,Mitundu iwiri iri m'mimba mwako,Magulu awiri a anthu adzaturuka m'mimba mwako;Gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzace;Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.
24 Atatha masiku ace akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.
25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwace monga maraya aubweya; ndipo anamucha dzina lace Esau.
26 Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.
27 Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.