24 Atatha masiku ace akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.
25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwace monga maraya aubweya; ndipo anamucha dzina lace Esau.
26 Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.
27 Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.
28 Ndipo Isake anakonda Esau, cifukwa anadya nyama yace ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo,
29 Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anacokera kuthengo, nalefuka:
30 ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye cofiiraco; cifukwa ndalefuka: cifukwa cace anamucha dzina lace Edomu.