11 Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.
12 Ndipo Isake anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi caka cimeneco; ndipo Yehova anamdalitsa iye.
13 Ndipo anakula munthuyo, nakulakula kufikira kuti anakhala wamkurukuru:
14 ndipo anali ndi cuma ca nkhosa, ndi cuma ca zoweta, ndi banja lalikuru: ndipo Afilisti anamcitira iye nsanje.
15 Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wace Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.
16 Ndipo Abimeleke anati kwa Isake, Ucoke kwa ife cifukwa kuti iwe uti wamkuru wopambana ife.
17 Ndipo Isake anacoka kumeneko, namanga hema wace m'cigwa ca Gerari, nakhala kumeneko.