26 Ndipo ananka kwa iye Abimeleke kucokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lace, ndi Fikoli, kazembe wa nkhondo yace.
27 Ndipo Isake anati kwa iwo, Mwandidzera cifukwa ciani, inu akundida ine, ndi kundicotsa kwanu?
28 Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, ticite pangano ndi iwe;
29 kuti usaticitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakucirira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.
30 Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.
31 Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzace; ndipo Isake anawalola amuke, ndipo anauka kucokera kwa iye m'mtendere.
32 Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ace a Isake anadza namuuza iye za citsime cimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.