27 Ndipo Isake anati kwa iwo, Mwandidzera cifukwa ciani, inu akundida ine, ndi kundicotsa kwanu?
28 Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, ticite pangano ndi iwe;
29 kuti usaticitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakucirira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.
30 Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.
31 Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzace; ndipo Isake anawalola amuke, ndipo anauka kucokera kwa iye m'mtendere.
32 Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ace a Isake anadza namuuza iye za citsime cimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.
33 Ndipo anacha dzina lace Seba, cifukwa cace dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino.