9 Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.
10 Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife:
11 Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.
12 Ndipo Isake anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi caka cimeneco; ndipo Yehova anamdalitsa iye.
13 Ndipo anakula munthuyo, nakulakula kufikira kuti anakhala wamkurukuru:
14 ndipo anali ndi cuma ca nkhosa, ndi cuma ca zoweta, ndi banja lalikuru: ndipo Afilisti anamcitira iye nsanje.
15 Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wace Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.