22 Ndipo Yakobo anasendera kwa Isake atate wace, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.
23 Ndipo sanazindikira iye, cifukwa kuti manja ace anali aubweya, onga manja a Esau mkuru wace; ndipo anamdalitsa iye.
24 Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? ndipo anati, Ndine amene.
25 Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.
26 Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.
27 Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zobvala zace, namdalitsa, nati,Taona, kununkhira kwa mwana wanga,Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
28 Mlungu akupatse iwe mame a kumwamba,Ndi zonenepa za dziko lapansi,Ndi tirigu wambiri ndi vinyo;