1 Ndipo Isake anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani.
2 Tauka, nupite ku Padanaramu, ku nyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana akazi a Labani mlongo wace wa amako.
3 Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akucurukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:
4 akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.
5 Ndipo Isake anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wace wa Betuele Msuriya, mlongo wace wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.
6 Ndipo anaona Esau kuti Isake anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko;
7 ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani; ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wace ndi amace, nanka ku Padanaramu;