17 Maso a Leya anali ofok a, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.
18 Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.
19 Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine.
20 Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka cifukwa ca cikondi cimene anamkonda iye naco.
21 Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse Ine mkazi wanga, cifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.
22 Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.
23 Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wace wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo.