17 Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkuru wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? za yani zimenezi patsogolo pako?
18 pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.
19 Ndipo anauzanso waciwiri ndi wacitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau cotero, pamene mukomana naye:
20 ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu, Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pace ndidzaona nkhope yace; kapena adzandilandira ine.
21 Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pace: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pacigono.
22 Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ace awiri, ndi adzakazi ace awiri, ndi ana ace amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa doko la Yaboki.
23 Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonseanalinazo.