2 Ndipo Yakobo anati kwa a banja lace, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Cotsani milungu yacilendo iri mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zobvala zanu:
3 tinyamuke, tikwere tinke ku Beteli: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandibvomereza tsiku la mabvuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo.
4 Ndipo anampatsa Yakobo milungu yacilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.
5 Ndipo anapita, ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera midzi yakuwazinga, ndipo sanalondola ana a Yakobo.
6 Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Beteli), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye.
7 Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, Dacha pamenepo El Beteli: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wace.
8 Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Beteli, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anacha dzina lace AlioniBakuti.