7 Cifukwa cuma cao cinali cambiri cotero kuti sanakhoza kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira cifukwa ca ng'ombe zao.
8 Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.
9 Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi:
10 amenewa ndi maina a ana amuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wace wa Esau, Reueli mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wace wa Esau.
11 Ndipo ana amuna a Elifazi ndiwo Temani, Omari, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi.
12 Ndipo Timna anali mkazi wace wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleki: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wace wa Esau.
13 Ndi ana amuna a Reueli: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wace wa Esau.