4 Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pace, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, naika m'manja mwace zonse anali nazo.
5 Ndipo panali ciyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, ndi pa zace zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto cifukwa ca Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zace zonse, m'nyumba ndi m'munda.
6 Ndipo iye anasiya zace zonse m'manja a Yosefe; osadziwa comwe anali naco, koma cakudya cimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.
7 Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyace anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
8 Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyace, Taonani, mbuyanga sadziwa cimene ciri ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zace zonse m'manja anga;
9 mulibe wina m'nyumba wamkuru ndine; ndipo sanandikaniza ine kanthu, koma iwe, cifukwa kuti uli mkazi wace: nanga ndikacita coipa cacikuru ici bwanji ndi kucimwira Mulungu?
10 Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvera mkazi kugona naye kapena kukhala naye.