12 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yace: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi.
13 Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukuru kosapiririka.
14 Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.
15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Cifukwa cace ali yense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika icizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe ali yense akampeza.
16 Ndipo Kaini anaturuka pamaso pa Yehova, ndipo anakhalam'dziko la Nodi, kum'mawa kwace kwa Edene.
17 Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.
18 Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.