15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Cifukwa cace ali yense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika icizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe ali yense akampeza.
16 Ndipo Kaini anaturuka pamaso pa Yehova, ndipo anakhalam'dziko la Nodi, kum'mawa kwace kwa Edene.
17 Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.
18 Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.
19 Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lace la wina ndi Ada, dzina lace la mnzace ndi Zila.
20 Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe,
21 Ndi dzina la mphwace ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oyimba zeze ndi citoliro.