49 Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mcenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; cifukwa anali wosawerengeka.
50 Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana amuna awiri, cisanafike caka ca njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Porifera wansembe wa Oni anambalira iye.
51 Ndipo Yosefe anamucha dzina la woyamba Manase, cifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zobvuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.
52 Ndipo dzina la waciwiri anamucha Efraimu: cifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.
53 Ndipo zaka zakucuruka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Aigupto, zinatha.
54 Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Aigupto munali cakudya.
55 Ndipo pamene dziko lonse la Aigupto linali ndi njala, anthu anapfuulira Farao awapatse cakudya; ndipo Farao anati kwa Aaigupto onse, Pitani kwa Yosefe: cimene iye anena kwa inu citani.