19 Mbuyanga anafunsa akapolo ace kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu?
20 Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tiri ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wace wamng'ono; mbale wace wafa, ndipo iye yekha watsala wa amace, ndipo atate wace amkonda iye.
21 Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.
22 Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wace; pakuti akamsiya atate wace, atate wace adzafa.
23 Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga,
24 Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanus atate, wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.
25 Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife cakudya pang'ono.