3 Pamene kudaca, anamukitsa anthu iwo ndi aburu ao.
4 Ataturuka m'mudzi asanamuke patari, Yosefe anati kwa tsanyumba wace, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Cifukwa canji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?
5 Kodi si ndico comwera naco mbuyanga, naombeza ula naco? Mwacitira coipa pakutero.
6 Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo.
7 Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu acite cotero?
8 Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kuturuka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golidi?
9 iye wa akapolo anu ampeza naco afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.