9 iye wa akapolo anu ampeza naco afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.
10 Ndipo iye mati, Tsononso cikhale monga mwa nau anu: iye amene ampeza naco adzakhala kapolo wanga; ndipo inu nudzakhala opanda cifukwa.
11 Ndipo anafulumira natsitsa pansi zense thumba lace, namasula yense humba lace.
12 Ndipo iye anafunauna kuyambira pa wamkuru naleka pa wamng'ono; nacipeza cikho n'thumba la Benjamini:
13 ndipo anang'amba zobvala zao, nasenzetsa yense buru wace, nabwera kumuzi.
14 Yudanso ndi abale ace anadza cu nyumba ya Yosefe; ndipo iye ikali pamenepo; ndipo anagwa oansi patsogolo pace.
15 Ndipo losefe anati kwa iwo, Ici nciani nwacicita? Kodi simudziwa kuti nunthu ngati ine ndingathe kuzindidra ndithu?