1 Ndipo Israyeli anamuka ulendo wace ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isake atate wace.
2 Ndipo Mulungu ananena kwa Israyeli, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.
3 Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Aigupto; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukuru;
4 Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Aigupto; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lace pamaso pako.
5 Ndipo Yakobo anacoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israyeli anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magareta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye,
6 Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi cuma cao anacipezam'dziko la Kanani, nadza ku Aigupto, Yakobo ndi mbeu zace zonse pamodzi ndi iye;