9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo angam'masikua ulendowao.
10 Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, naturuka pamaso pa Farao.
11 Ndipo Yosefe anakhazika atate wace ndi abale ace, napatsa iwo pokhala m'dziko la Aigupto, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramese, monga analamulira Farao.
12 Ndipo Yosefe anacereza atate wace ndi abale ace, ndi mbumba yonse ya atate wace ndi cakudya monga mwa mabanja ao.
13 Ndipo munalibe cakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; cifukwa cace dziko la Aaigupto ndi dziko la Kanani unalefuka cifukwa ca njalayo.
14 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama ku nyumba ya Farao.
15 Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, Aaigupto onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife cakudya; tiferenji pamaso panu? zatsirizika ndalama.