9 Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.
10 Koma maso a Israyeli anali akhungu m'ukalamba wace, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.
11 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndione nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.
12 Ndipo Yosefe anaturutsa iwo pakati pa maondo ace, nawerama ndi nkhope yace pansi.
13 Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efraimu m'dzanja lace lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lace lamanzere ku dzanja lamanja la Israyeli, nadza nao pafupi ndi iye.
14 Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lace lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lace lamanzere pa mutu wa Manase anapingasitsa manja ace dala; cifukwa Manase anali woyamba.
15 Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pace anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isake, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,